1 Samuel 25:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muŵafunse antchito anuwo, adzakuuzani. Nchifukwa chake muŵakomere mtima anyamata anga, pakuti tabwera nthaŵi ino yachikondwerero. Chonde muŵapatse anyamata angaŵa ndi ine bwenzi lanu Davide, chilichonse chimene mungakhale nacho.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mufunse anyamata anu, adzakuuzani; chifukwa chake muwakomere mtima anyamata awa, pakuti tilikufika tsiku labwino; mupatse chilichonse muli nacho m'dzanja lanu, kwa anyamata anu, ndi kwa mwana wanu Davide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muwafunse antchito anu ndipo akuwuzani. Kotero akomereni mtima anyamata anga, pakuti tabwera pa nthawi yachikondwerero. Chonde apatseniko antchito anuwo ndi mwana wanu Davide chilichonse chimene mungakhale nacho.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mufunse anyamata anu, adzakuuzani; cifukwa cace muwakomere mtima anyamata awa, pakuti tirikufika tsiku labwino; mupatse ciri conse muli naco m'dzanja lanu, kwa anyamata anu, ndi kwa mwana wanu Davide.