1 Samuel 26:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta andiletse kuti ndisapweteke wodzodzedwa wake. Koma tsono tingotenga mkondo umene uli kumutu kwakewu ndi mtsuko wa madziwu, ndipo tizipita.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova; koma utenge mkondowo uli kumutu kwake, ndi chikho cha madzi, ndipo tiyeni, timuke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova andiletse kuti ndisapweteke wodzozedwa wa Yehova. Tsopano tingotenga mkondo umene uli ku mutu kwakewo ndi botolo la madzilo ndipo tizipita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova; koma utenge mkondowo uli kumutu kwace, ndi cikho ca madzi, ndipo tiyeni, timuke.