1 Samuel 26:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Davide adatenga mkondo ndi mtsuko wa madzi, zimene zinali kumutu kwa Saulo, nachokapo. Palibe amene adaona zimenezo ngakhale kuzidziŵa, ndipo panalibe wina aliyense amene adadzuka. Onse anali m'tulo, chifukwa chakuti Chauta adaaŵagonetsa tulo tofa nato.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho Davide anatenga mkondowo, ndi chikho cha madzi ku mutu wa Saulo nachoka iwowa, osawaona munthu, kapena kuzidziwa, kapena kugalamuka; pakuti onse anali m'tulo; popeza tulo tatikulu tochokera kwa Yehova tinawagwira onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero Davide anatenga mkondo ndi botolo lamadzi zimene zinali ku mutu kwa Sauli ndipo anachoka. Palibe amene anaona zimenezi kapena kudziwa, ndipo palibenso amene anadzuka. Onse anali mʼtulo, chifukwa Yehova anawagonetsa tulo tofa nato.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco Davide anatenga mkondowo, ndi cikho ca madzi ku mutu wa Sauli nacoka iwowa, osawaona munthu, kapena kuzidziwa, kapena kugalamuka; pakuti onse anati m'tulo; popeza tulo tatikuru tocokera kwa Yehova tinawagwira onse.