1 Samuel 26:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene wachitazi si zabwino ai. Pali Chauta wamoyo, nonsenu muyenera kuphedwa chifukwa simudalonde mbuye wanu, wodzozedwa wa Chauta. Uyang'ane kumene kuli mkondo wa mfumu ndi mtsuko wa madzi, zimene zinali kumutu kwake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ichi unachichita sichili chabwino. Pali Yehova, muyenera kufa inu, chifukwa simunadikira mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Ndipo tsono, penyani mkondo wa mfumu ndi chikho cha madzi zinali kumutu kwake zili kuti?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chimene wachita iwe si chabwino. Pali Yehova wamoyo iwe ndi asilikali ako muyenera kufa chifukwa simunateteze mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Tayangʼanayangʼana. Uli kuti mkondo wa mfumu ndi botolo lamadzi zimene zinali kumutu kwa mfumu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ici unacicita siciri cabwino. Pali Yehova, muyenera kufa inu, cifukwa simunadikira mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Ndipo tsono, penyani mkondo wa mfumu ndi cikho ca madzi zinali kumutu kwace ziri kuti?