1 Samuel 26:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake tsono, mbuyanga mfumu, mumve mau a ine mtumiki wanu. Ngati ndi Chauta amene wautsa mtima wanu kuti mundiwukire, Chautayo apepesedwe ndi nsembe. Koma ngati ndi anthu, iwowo Chauta aŵatemberere, pakuti tsono andipirikitsa, kuti ndisakhale nao m'dziko la Chauta. Akuti, ‘Pita katumikire milungu ina.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano mbuye wanga mfumu tamverani mawu a mtumiki wanu. Ngati ndi Yehova wautsa mtima wanu kuti mundiwukire, ndiye alandire chipepeso. Koma ngati ndi anthu amene achita zimene, ndiye Yehova awatemberere popeza andipirikitsa lero kundichotsa mʼdziko la Yehova, namati, ‘Pita kapembedze milungu ina.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wace. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire copereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipitikitsa lero kuti ndisalandireko colowa ca Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu yina.