1 Samuel 26:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamanga zithando zankhondo pa phiri la Hakila, limene lili pambali pa mseu, chakuvuma kwa Yesimoni. Koma Davide adakhalabe kuchipululuko. Tsono ataona kuti Saulo akumlondola,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Saulo namanga zithando m'phiri la Hakila kupenya kuchipululu kunjira. Koma Davide anakhala kuchipululu, naona kuti Saulo alikumfuna kuchipululu komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli anamanga msasa wake mʼmbali mwa njira yopita ku phiri la Hakila moyangʼanana ndi Yesimoni. Koma Davide anali mʼchipululumo. Davide ataona kuti Sauli amamulondola mpaka kumeneko,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sauli namanga zithando m'phiri la Hagila kupenya kucipululu kunjira, Koma Davide anakhala kucipululu, naona kuti Sauli alikumfuna kucipululu komweko.