1 Samuel 26:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye Davide adanyamuka nakafika pa malo amene Saulo adaamangapo zithando zake. Ndipo adaona malo amene ankagonapo Sauloyo ndi Abinere mwana wa Nere, mkulu wa ankhondo a Saulo. Sauloyo ankagona m'zithandomo, ndipo gulu lonse lankhondo lidaamanga zithando pomzungulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo paja Saulo anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Saulo, ndi Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu lake; ndipo Saulo anagona pakati pa linga la magaleta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Davide ananyamuka napita kumalo kumene Sauli anamanga misasa. Iye anaona pamene Sauli ndi Abineri mwana wa Neri mkulu wa ankhondo anagona. Sauli anagona mʼkati mwa tenti ndipo asilikali anagona momuzungulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo pala Sauli anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Sauli, ndi Abineri mwana wa Neri kazembe wa khamu lace; ndipo Sauli anagona pakati pa linga la magareta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pace.