1 Samuel 26:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adafunsa Ahimeleki Muhiti ndi Abisai mkulu wa Yowabu, mwana wa Zeruya, kuti, “Kodi ndani apite nane ku zithando za Saulo?” Abisai adati, “Ine ndipita nanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Muhiti, ndi Abisa, mwana wa Zeruya, mbale wake wa Yowabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Saulo? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Davide anafunsa Ahimeleki Mhiti ndi Abisai mwana wa Zeruya, mʼbale wa Yowabu kuti, “Ndani adzapita nane ku msasa kwa Sauli?” Abisai anayankha kuti, “Ine ndidzapita nanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Mhiti, ndi Abisai mwana wa Zeruya, mbale wace wa Yoabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Sauli? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.