1 Samuel 26:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abisai adauza Davide kuti, “Mulungu wapereka mdani wanu kwa inu lero. Bwanji tsono mundilole kuti ndimbaye ndi mkondo kamodzinkamodzi ndi kumkhomerera pansi, sindichita kumbaya kaŵiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m'dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abisai anawuza Davide kuti, “Lero Mulungu wapereka mdani wanu mʼmanja mwanu. Tsopano ndiloleni ndimukhomere pansi ndi mkondo wangawu kamodzinʼkamodzi. Sindimulasa kawiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m'dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri.