1 Samuel 27:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adaganiza mumtima mwake kuti, “Tsiku lina Saulo adzandipha. Palibe china chimene ndingachitepo, koma kuthaŵira ku dziko la Afilisti. Choncho Saulo adzaleka kumandifunafuna m'dziko la Aisraele, ndipo ndidzapulumuka kwa iye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anaganiza mu mtima mwake nati, “Tsiku lina ine ndidzaphedwa ndi Sauli. Palibe chabwino ndingachite, koma kuthawira ku dziko la Afilisti. Kotero Sauli adzasiya kundifunafuna mʼdziko lonse la Israeli, ndipo ndidzapulumuka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ananena mumtima mwace, Tsiku tina Sauli adzandipha; palibe cina condikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Sauli adzakhala kakasi cifukwa ca ine, osandifunanso m'malire onse a Israyeli, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lace.