1 Samuel 27:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akisi akafunsa kuti, “Kodi munakamenya nkhondo ndi yani lero?” Davide ankati, “Tinakamenya nkhondo kumwera kwa Yuda,” mwina ankati, “Ku dziko la Ayeramiyele,” mwina ankati, “Ku dziko la Akeni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Akisi anati, Waponyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameele, ndi a kumwera kwa Akeni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akisi akafunsa kuti, “Kodi lero unapita kukathira nkhondo kuti?” Davide ankayankha kuti, “Ndinapita kukathira nkhondo kummwera kwa Yuda,” mwinanso ankanena kuti, “Ndinapita ku dziko la Ayerahimeeli” kapenanso ankanena kuti, “Ndinapita ku dziko la Akeni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Akisi anati, Wapooyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameli, ndi a kumwera kwa Akeni.