1 Samuel 27:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Davide adauza Akisi kuti, “Ngati ndapeza kuyanja pamaso panu, mundipatse malo pa mudzi wina m'dziko mwanu kuti ndizikhala kumeneko. Kodi ine mtumiki wanu ndizikhaliranji pamodzi ndi inu mu mzinda wanu waufumu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kumilaga, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji m'mudzi wachifumu pamodzi ndi inu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Davide anawuza Akisi kuti, “Ngati ndapeza kuyanja pamaso panu mundipatse malo dera limodzi la dziko lanu kuti ndizikhala kumeneko. Mtumiki wanu adzakhala mu mzinda waufumu chifukwa chiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kumiraga, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji m'mudzi wacifumu pamodzi ndi inu?