1 Samuel 27:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide ndi anthu amene anali naye ankapita kwa Agesuri, Agerizi, ndi Aamaleke nakaŵathira nkhondo onsewo. Mitundu imeneyi inali nzika za dzikolo kuyambira kale. Dziko lao linkafika ku Suri ndipo linkachita malire ndi dziko la Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ndi anthu ake anakwera, nathira nkhondo yovumbulukira pa Agesuri, ndi Agerizi, ndi Aamaleke; pakuti awa ndiwo anthu akale m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Davide ndi anthu ake ankapita kukathira nkhondo Agesuri, Agirizi ndi Aamaleki. (Mitundu ya anthu imeneyi kuyambira kale inkakhala mʼdziko la pakati pa Suri ndi Igupto).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ndi anthu ace anakwera, nathira nkhondo yobvumbulukira pa Agesuri, ndi Agirezi, ndi Aamaleki; pakuti awa ndiwo anthu akale a m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Aigupto.