1 Samuel 27:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa maulendo ake ankhondowo Davide ankapha anthu a m'dzikolo, osasiyapo wamoyo mwamuna kapena mkazi. Koma ankatenga nkhosa, ng'ombe, abulu, ngamila, ndi zovala, ndipo zonsezo ankabwerera nazo kwa Akisi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anapasula dzikolo, sanasunge ndi moyo mwamuna kapena wamkazi; natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi ngamira, ndi zovala; nabwera nafika kwa Akisi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide ankati akathira nkhondo dera lina, sankasiya munthu wamoyo, mwamuna kapena mkazi, koma ankatenga nkhosa, ngʼombe, abulu, ngamira ndi zovala, pambuyo pake nʼkubwerera kwa Akisi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anapasula dzikolo, sanasunga ndi moyo mwamuna kapena wamkazi; natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi aburu, ndi ngamila, ndi zobvala; nabwera nafika kwa Akisi.