1 Samuel 28:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ina Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo, kuti amenyane ndi Aisraele. Tsono Akisi adauza Davide kuti, “Udziŵe kuti iwe ndi anthu ako muyenera kupita nane ku nkhondo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali masiku aja, Afilisti anasonkhanitsa pamodzi makamu ao onse kunkhondo, kuti akaponyane ndi Aisraele. Ndipo Akisi ananena ndi Davide, Dziwa kuti zoonadi, udzatuluka nane ndi nkhondo, iwe ndi anthu ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmasiku amenewo Afilisti anasonkhanitsa ankhondo awo kuti akamenyane ndi Aisraeli. Akisi anawuza Davide kuti, “Udziwe kuti iwe pamodzi ndi anthu ako mudzapita nane ku nkhondo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali masiku aja, Afilisti anasonkhanitsa pamodzi makamu ao onse kunkhondo, kuti akaponyane ndi Aisrayeli. Ndipo Akisi ananena ndi Davide, Dziwa kuti zoonadi, udzaturuka nane ndi nkhondo, iwe ndi anthu ako.