1 Samuel 28:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mkaziyo adaona Samuele, adakuwa kwambiri nati, “Chifukwa chiyani mwandinyenga? Ndinu mfumu Saulo!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkaziyo pakuona Samuele, anafuula ndi mau akulu; ndi mkaziyo analankhula ndi Saulo, nati, Munandinyengeranji? Popeza inu ndinu Saulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene mkaziyo anaona Samueli anakuwa kwambiri, nawuza Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani inu mwandipusitsa? Inu ndinu Sauli!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkaziyo pakuona Samueli, anapfuula ndi mau akuru; ndi mkaziyo analankhula ndi Sauli, nati, Munandinyengeranji? popeza inu ndinu Sauli.