1 Samuel 28:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saulo adafunsa mkaziyo kuti, “Kodi maonekedwe a mzimuwo ngotani?” Mkaziyo adati, “Imene ikutuluka ndi nkhalamba, yavala mkanjo.” Apo Saulo adadziŵa kuti ndi Samuele ameneyo, ndipo adapereka ulemu pakuŵerama ndi kugunditsa nkhope yake pansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena naye, Makhalidwe ake ndi otani? Nati iye, Nkhalamba ilikukwera yovala mwinjiro. Pamenepo Saulo anazindikira kuti ndi Samuele, naweramitsa nkhope yake pansi, namgwadira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli anafunsa, “Kodi mzimuwo ukuoneka motani?” Mkaziyo anayankha kuti, “Amene akutuluka ndi munthu wokalamba ndipo wavala mkanjo.” Apo Sauli anadziwa kuti anali Samueli ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena naye, Makhalidwe ace ndi otani? nati iye, Nkhalamba irikukwera yobvala mwinjiro. Pamenepo Sauli anazindikira kuti ndi Samueli, naweramitsa nkhope yace pansi, namgwadira.