1 Samuel 28:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Samuele adafunsa Saulo kuti, “Chifukwa chiyani wandivuta ponditulutsa kuti ndibwere kuno?” Saulo adayankha kuti, “Ndavutika kwambiri, pakuti Afilisti abwera kudzandithira nkhondo, ndipo Mulungu wandifulatira osandiyankhanso, ngakhale podzera mwa aneneri, kapena m'maloto. Nchifukwa chake ndakuitanani kuti mundiwuze zomwe ndiyenera kuchita.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Samueli anafunsa Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandivutitsa pondiyitana kuti ndibwere kuno?” Sauli anayankha kuti, “Ine ndavutika kwambiri mʼmaloto. Afilisti akumenyana nane, ndipo Mulungu wandifulatira. Iye sakundiyankhulanso, ngakhale kudzera mwa aneneri kapena maloto. Choncho ndakuyitanani kuti mundiwuze zoti ndichite.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Wandibvutiranji kundikweretsa kuno? Sauli nayankha, Ndirikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandicokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; cifukwa cace ndakuitanani, kuti mundidziwitse cimene ndiyenera kucita.