1 Samuel 28:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta wakuchita zomwe adakuuza kudzera mwa ine. Wakulanda ufumu, waupereka kwa wina, kwa Davide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova yekha wachita monga ananena pakamwa panga; ndipo Yehova wang'amba ufumuwo, kuuchotsa m'dzanja lako, ndi kuupatsa mnansi wako, ndiye Davide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova wakuchita zimene ananeneratu kudzera mwa ine. Yehova wachotsa ufumu mʼmanja mwako ndipo waupereka kwa mnansi wako, kwa Davide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova yekha wacita monga ananena pakamwa panga; ndipo Yehova wang'amba ufumuwo, kuucotsa m'dzanja lako, ndi kuupatsa mnansi wako, ndiye Davide.