1 Samuel 28:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adayankha kuti, “Chabwino, mudzaona zimene ndichite ine mtumiki wanu.” Akisi adati, “Chabwino, ndidzakuika kuti ukhale mlonda wonditchinjiriza pa moyo wako wonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anati kwa Akisi, Potero mudzadziwe chimene mnyamata wanu adzachita. Ndipo Akisi anati kwa Davide, Chifukwa chake ndidzakuika iwe ukhale wondisungira moyo wanga masiku onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anayankha kuti, “Tsono inu mudzaona zimene mtumiki wanune ndingachite.” Akisi anayankha kuti, “Chabwino ine ndidzakuyika iwe kukhala mlonda wanga moyo wako wonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anati kwa Akisi, Potero mudzadziwe cimene mnyamata wanu adzacita. Ndipo Akisi anati kwa Davide, Cifukwa cace ndidzakuika iwe ukhale wondisungira moyo wanga masiku onse.