1 Samuel 28:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mkazi uja adasendera pafupi ndi Saulo, ndipo ataona kuti akuchita mantha, adamuuza kuti, “Taonani, mdzakazi wanune ndakumverani. Ine ndataya moyo wanga pomvera zimene munandiwuza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkaziyo anafika kwa Saulo, naona kuti ali wovutika kwambiri, nanena naye, Onani, mdzakazi wanu anamvera mau anu, ndipo ndinataya moyo wanga, ndi kumvera mau anu munalankhula ndi ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkazi uja tsono anasendera kufupi ndi Sauli, ndipo ataona kuti Sauli akuchita mantha, anamuwuza kuti, “Taonani, mdzakazi wanune ndakumverani. Ndayika moyo wanga pa chiswe ndipo ndamvera zimene munandiwuza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkaziyo anafika kwa Sauli, naona kuti ali wobvutika kwambiri, nanena naye, Onani, mdzakazi wanu anamvera mau anu, ndipo ndinataya moyo wanga, ndi kumvera mau anu munalankhula ndi ine.