1 Samuel 28:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake tsono, inunso mumvere mau anga. Mundilole ndikuikireni kabuledi pang'ono, mudye kuti muwone nyonga zoyendera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsono, mumverenso mau a mdzakazi wanu, nimundilole kuika kakudya pamaso panu; ndipo mudye, kuti mukhale ndi mphamvu pakumuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono inunso mumvere mawu a mdzakazi wanune. Mundilole kuti ndikupatseni ka buledi pangʼono kuti mukhale ndi mphamvu zoyendera pa ulendo wanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsono, mumverenso mau a mdzakazi wanu, nimundilole kuika kakudya pamaso panu; ndipo mudye, kuti mukhale ndi mphamvu pakumuka.