1 Samuel 28:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapempha nzeru kwa Chauta, koma sadamuyankhe ngakhale podzera m'maloto, kapena mwa Urimu kapena mwa aneneri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Saulo anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankhe ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Sauli anafunsa nzeru kwa Yehova koma Yehova sanamuyankhe ngakhale kudzera mʼmaloto, kapena mwa Urimu ngakhalenso kudzera mwa aneneri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Sauli anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankha ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri.