1 Samuel 28:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Saulo adadzizimbaitsa, navala zovala zachilendo, napita. Pamodzi ndi anthu aŵiri adakafika kwa mkaziyo usiku. Ndipo adamuuza kuti, “Undifunsire zam'tsogolo kwa mizimu, makamaka undiitanire mzimu wa amene ndimtchule.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anadzizimbaitsa navala zovala zina, nanka iye pamodzi ndi anthu ena awiri, nafika kwa mkaziyo usiku; nati iye, Undilotere ndi mzimu wobwebwetawo, nundiukitsire aliyense ndidzakutchulira dzina lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero Sauli anadzizimbayitsa navala zovala zachilendo. Tsono iye pamodzi ndi anthu awiri anapita nakafika kwa mkazi uja usiku, ndipo anamupempha kuti, “Chonde ndifunsireni nzeru kwa mizimu ya anthu akufa. Koma makamaka munditulutsire mzimu wa amene ndimutchule.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli anadzizimbaitsa nabvala zobvala zina, nanka iye pamodzi ndi anthu ena awiri, nafika kwa mkaziyo usiku; nati iye, Undilotere ndi mzimu wobwebwetawo, nundiukitsire ali yense ndidzakuchulira dzina lace.