1 Samuel 28:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkaziyo adati, “Inutu mukudziŵa zimene adachita mfumu Saulo. Suja adachotsa m'dziko muno anthu olankhula ndi mizimu ndiponso oombeza? Chifukwa chiyani tsono mukunditchera msampha kuti mundiphe?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkaziyo ananena naye, Onani, mudziwa chimene anachita Saulo, kuti analikha m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula; chifukwa ninji tsono mulikutchera moyo wanga msampha, kundifetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mkaziyo anayankha kuti, “Ndithu inu mukudziwa chimene Sauli anachita. Paja iye anachotsa mʼdziko muno anthu onse owombeza ndi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Chifukwa chiyani mukutchera moyo wanga msampha kuti ndiphedwe?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkaziyo ananena naye, Onani, mudziwa cimene anacita Sauli, kuti analikha m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula; cifukwa ninji tsono mulikuchera moyo wanga msampha, kundifetsa.