1 Samuel 29:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono udzuke m'mamaŵa, pamodzi ndi anthu ako amene udabwera nawo, munyamuke kukangocha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ulawirire m'mawa pamodzi ndi anyamata a mbuye wako amene anabwera nawe; ndipo mutauka m'mawa, mumuke kutacha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono udzuke mmamawa, pamodzi ndi ankhondo ako amene unabwera nawo, ndipo unyamuke kukangocha.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ulawirire m'mawa pamodzi ndi anyamata a mbuye wako amene anabwera nawe; ndipo mutauka m'mawa, mumuke kutaca.