1 Samuel 29:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Davide ndi anthu omwe anali naye adanyamuka m'mamaŵa nabwerera ku dziko la Afilisti. Koma Afilisti adakafika mpaka ku Yezireele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho Davide analawirira, iye ndi anthu ake, kuti amuke m'mawa ndi kubwera ku dziko la Afilisti. Ndipo Afilisti anakwera Yezireele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Davide ndi anthu ake anadzuka mmamawa kubwerera ku dziko la Afilisti. Koma Afilistiwo anapita ku Yezireeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco Davide analawirira, iye ndi anthu ace, kuti amuke m'mawa ndi kubwera ku dziko la Afilisti. Ndipo Afilisti anakwera ku Jezreeli.