1 Samuel 29:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iwo adamkalipira Akisiyo namuuza kuti, “Mumbweze munthuyo kuti abwerere ku malo amene mudampatsa. Sadzapita nafe ku nkhondo, kuwopa kuti kunkhondoko angakasanduke mdani wathu. Nanga munthu ameneyu angathe kudziyanjanitsa bwanji ndi mbuyake? Iyeyu angathe kuchita zimenezi pakupha anthu athu ali panoŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma akalonga a Afilisti anapsa naye mtima; nanena naye akalonga a Afilisti, Bwezani munthuyu, abwerere kumalo kwake kumene munamuikako, asatsikire nafe kunkhondo, kuti kunkhondoko angasanduke mdani wathu; pakuti uyu adzadziyanjanitsa ninji ndi mfumu yake? Si ndi mitu ya anthu awa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma atsogoleri a ankhondo a Afilisti anamukwiyira Akisi kwambiri ndipo anati, “Mubweze munthuyu kuti abwerere ku malo amene unamupatsa. Iye asapite nafe ku nkhondo kuopa kuti angadzasanduke mdani wathu. Kodi iyeyu adzadziyanjanitsa bwanji ndi mbuye wake? Iyeyutu adzadziyanjanitsa ndi mbuye wake pakupha anthu ali panowa?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma akalonga a Afilisti anapsa naye mtima; nanena naye akalonga a Afilisti, Bwezani munthuyu, abwerere kumalo kwace kumene munamuikako, asatsikire nafe kunkhondo, kuti kunkhondoko angasanduke mdani wathu; pakuti uyu adzadziyanjanitsa ninji ndi mfumu yace? Si ndi mitu ya anthu awa?