1 Samuel 29:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Akisi adaitana Davide namuuza kuti, “Pali Chauta wamoyo, iwe wakhala wokhulupirika kwa ine, ndipo kutumikira kwako m'magulu anga ankhondo kwandikomera kwambiri. Sindidakupeze cholakwa kuyambira tsiku limene udabwera kuno mpaka lero lino. Komabe atsogoleri enaŵa sakukufuna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Akisi anaitana Davide, nanena naye, Pali Yehova, wakhala woongoka mtima, ndipo kutuluka kwako ndi kubwera kwako pamodzi ndi ine m'gulumo kundikomera; pakuti sindinaona choipa mwa iwe kuyambira tsiku la kufika kwako kufikira lero; koma akalongawo sakukomera mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero Akisi anayitana Davide ndipo anamuwuza kuti, “Pali Yehova wamoyo, iwe wakhala wodalirika ndipo chikanakhala chinthu chabwino kuti uzimenya nkhondo pamodzi nane popeza chibwerere iwe kuno ine sindinapeze cholakwa chilichonse ndi iwe. Koma atsogoleri enawa ndiwo sakukufuna.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Akisi anaitana Davide, nanena naye, Pali Yehova, wakhala woongoka mtima, ndipo kuturuka kwako ndi kubwera kwako pamodzi ndi ine m'gulumo kundikomera; pakuti sindinaona coipa mwa iwe kuyambira tsiku la kufika kwako kufikira lero; koma akalongawo sakukomera mtima.