1 Samuel 29:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adamufunsa kuti, “Kodi ndachita chiyani? Kodi mwapeza chiyani pa ine mtumiki wanu, kuyambira nthaŵi imene ndidayamba kukugwirirani ntchito mpaka tsopano lino? Nanga ndilekerenji kukamenyana nkhondo ndi adani anu, mbuyanga mfumu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananena ndi Akisi, Koma ndinachitanji? Ndipo munapeza chiyani mu mnyamata wanu nthawi yonse ndili pamaso panu kufikira lero, kuti sindingapite kukaponyana nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anafunsa Akisi kuti, “Kodi ndachita chiyani? Kodi mwapeza cholakwa chotani mwa ine mtumiki wanu chiyambire kukutumikirani mpaka lero? Tsono chifukwa chiyani sindingapite kukamenya nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ananena ndi Akisi, Koma ndinacitanji? Ndipo munapeza ciani mu mnyamata wanu nthawi yonse ndiri pamaso panu kufikira lero, kuti sindingapite kukaponyana nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu?