1 Samuel 29:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akisi adayankha kuti, “Ndikudziŵa kuti ndiwe wosalakwa ndithu, monga mngelo wa Mulungu. Komabe atsogoleri ankhondo a Afilisti akunena kuti, ‘Davide asapite nafe ku nkhondo.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Akisi anayankha nanena ndi Davide, Ndidziwa kuti pamaso panga uli wabwino, ngati mthenga wa Mulungu; koma akalonga a Afilisti anena, Iye asamuke nafe kunkhondoko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akisi anayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti ndiwe wangwiro ngati mngelo wa Mulungu. Komabe atsogoleri a ankhondo a Afilisti akuti, ‘Davide asapite nafe ku nkhondo.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Akisi anayankha nanena ndi Davide, Ndidziwa kuti pamaso panga uli wabwino, ngati mthenga wa Mulungu; koma akalonga a Afilisti anena, iye asamuke nafe kunkhondoko.