1 Samuel 3:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adabwera nadzaimirira pomwepo, ndipo adaitananso monga nthaŵi zina zija kuti, “Samuele, Samuele!” Samuele adayankha kuti, “Lankhulani, poti mtumiki wanune ndilikumva.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samuele, Samuele. Pompo Samuele anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anabwera ndi kuyima pomwepo, ndi kuyitana monga nthawi zina zija, “Samueli! Samueli!” Ndipo Samueli anayankha, “Yankhulani, pakuti mtumiki wanu akumvetsera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samueli, Samueli. Pompo Samueli anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva.