1 Samuel 3:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikumdziŵitsa Eliyo kuti ndili pafupi kulanga banja lake mpaka muyaya, chifukwa cha zoipa zimene ana ake ankandichita. Eli ankazidziŵa zimenezo, koma osaŵaletsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yake kosatha chifukwa cha zoipa anazidziwa, popeza ana ake anadzitengera temberero, koma iye sanawaletse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ndinamudziwitsa kuti Ine ndikhoza kulanga banja lake kwamuyaya chifukwa cha zoyipa zimene ana ake ankadziyipitsa nazo. Iye ankadziwa zimenezi koma osawaletsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yace kosatha cifukwa ca zoipa anazidziwa, popeza ana ace anadzitengera temberero, koma iye sanawaletsa.