1 Samuel 3:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Samuele adagona mpaka m'maŵa. Atadzuka adatsekula zitseko za nyumba ya Chauta. Ankachita mantha kumuuza Eli zimene Chauta adaamuululirazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Samuele anagona kufikira m'mawa, natsegula zitseko za nyumba ya Yehova. Ndipo Samuele anaopa kudziwitsa Eli masomphenyawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Samueli anagona mpaka mmawa. Atadzuka anatsekula zitseko za Nyumba ya Yehova. Iye anachita mantha kumuwuza Eli za masomphenya ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Samueli anagona kufikira m'mawa, natsegula zitseko za nyumba ya Yehova. Ndipo Samueli anaopa kudziwitsa Eli masomphenyawo.