1 Samuel 3:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Eli adafunsa kuti, “Kodi nchiyani chimene Mulungu wakuuza? Usandibisire. Mulungu akulange ndithu, ukandibisira kanthu kalikonse pa zonse zimene wakuuza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Anakuuza chinthu chanji? Usandibisire ine. Mulungu akulange, ndi kuonjezapo, ngati undibisira chimodzi cha zonse zija adanena nawe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Eli anafunsa kuti, “Yehova wakuwuza chiyani? Usandibisire. Mulungu akulange ndithu ngati undibisira chilichonse cha zimene wakuwuza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Anakuuza cinthu canji? Usandibisire ine. Mulungu akulangendi kuonjezapo, ngati undibisira cimodzi ca zonse zija adanena nawe.