1 Samuel 3:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta ankadziwululabe ku Silo. Kumeneko ankamveketsa mau ake kwa Samuele polankhula naye. Ndipo mau ake a Samuele ankafika kwa Aisraele onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anaonekanso m'Silo, pakuti Yehova anadziwulula kwa Samuele ku Silo, mwa mau a Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anapitiriza kuoneka ku Silo, ndipo kumeneko anadziwulula yekha kwa Samueli mwa mawu ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anaonekanso m'Silo, pakuti Yehova anadziulula kwa Samueli ku Silo, mwa mau a Yehova.