1 Samuel 3:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Chauta adamuitananso kuti, “Samuele!” Pompo Samuele adadzuka napita kwa Eli nakamuuza kuti, “Ndabwera, ndamva ndithu kuitana.” Koma Eli adati, “Sindidakuitane mwana wanga, kagone.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samuele. Ndipo Samuele anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitana, mwana wanga; kagone.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anayitananso, “Samueli!” Ndipo Samueli anadzuka ndi kupita kwa Eli nati, “Ndabwera popeza ndamva mukundiyitana.” Eli nati, “Mwana wanga, ine sindinakuyitane, bwerera kagone.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samueli. Ndipo Samueli anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitana, mwana wanga; kagone.