1 Samuel 3:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adamuitananso Samuele kachitatu. Pompo adadzukanso, napita kwa Eli, nakanena kuti, “Ndabwera, mwandiitana ndithu basi.” Pamenepo Eli adazindikira kuti Chauta ndiye amene ankaitana mnyamatayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samuele nthawi yachitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anayitananso Samueli kachitatu ndipo Samueli anadzuka ndikupita kwa Eli ndipo anati, “Ndabwera popeza mwandiyitana ndithu.” Apo Eli anazindikira kuti Yehova ndiye ankayitana mnyamatayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samueli nthawi yacitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo.