1 Samuel 3:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adauza Samuele kuti, “Pita, kagone. Akakuitananso, ukanene kuti, ‘Lankhulani, Inu Chauta, poti mtumiki wanune ndilikumva.’ ” Choncho Samuele adapita kukagona kumalo kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Eli anati kwa Samuele, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukavomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Chomwecho Samuele anakagona m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Eli anamuwuza Samueli kuti, “Pita ukagone ndipo akakuyitananso ukanene kuti, ‘Yankhulani Yehova, pakuti mtumiki wanu ndikumvetsera.’ ” Choncho Samueli anapita ndi kukagona pamalo pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Eli anati kwa Samueli, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukabvomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Comweco Samueli anakagona m'malo mwace.