1 Samuel 30:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patapita masiku aŵiri, Davide ndi anthu ake adafika ku Zikilagi. Tsono adapeza kuti Aamaleke anali atasakaza dera la kumwera kwa Yuda ndi kuthira nkhondo mzinda wa Zikilagi. Adagonjetsa mzindawo, nauthira moto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ake ku Zikilagi tsiku lachitatu, Aamaleke adaponya nkhondo yovumbulukira kumwera, ndi ku Zikilagi, nathyola Zikilagi nautentha ndi moto;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lachitatu, Davide ndi anthu ake anakafika ku Zikilagi. Tsono anapeza Aamaleki atawononga kale dera la Negevi ndi Zikilagi. Anathira nkhondo mzinda wa Zikilagi ndi kuwutentha ndi moto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ace ku Zikilaga tsiku lacitatu, Aamaleki adaponya nkhondo yobvumbulukira kumwera, ndi ku Zikilaga, nathyola Zikilaga nautentha ndi moto;