1 Samuel 30:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamodzi ndi anthu 400 adapitirira kuŵalondola Aamalekewo, koma anthu 200 amene anali atatopa, adatsalira m'mbuyo, pakuti sadathe kuwoloka mtsinje wa Besori uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, chifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide ndi anthu ake 400 anapitirira kuwalondola Aamaleki aja. Koma anthu ena 200 anatsala popeza anatopa moti sakanatha kuwoloka mtsinje wa Besori uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, cifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori.