1 Samuel 30:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene anali ndi Davide, akuyenda m'njira, adapeza Mwejipito, nabwera naye kwa Davide. Tsono adampatsa buledi naadya. Adampatsanso madzi akumwa,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ena anapeza Mwejipito kuthengo, nabwera naye kwa Davide, nampatsa chakudya, nadya iye; nampatsanso madzi kumwa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amene anali ndi Davide anapeza Mwigupto mʼmunda wina ndipo anabwera naye kwa Davide. Iwo anamupatsa madzi kuti amwe ndi chakudya kuti adye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ena anapeza M-aigupto kuthengo, nabwera naye kwa Davide, nampatsa cakudya, nadya iye; nampatsanso madzi kumwa;