1 Samuel 30:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
chidutswa cha keke yankhuyu, ndi nchinchi ziŵiri za mphesa zoumika. Iyeyo atadya, moyo wake udatsitsimuka, pakuti sadaadya chakudya chilichonse, kapena kumwa madzi, masiku atatu athunthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nampatsanso chigamphu cha nchinchi ya nkhuyu ndi nchinchi ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wake unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya chakudya, osamwa madzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anamupatsanso chidutswa cha keke yankhuyu ndi makeke awiri a mphesa zowumika kuti adye. Atadya anapezanso mphamvu popeza anakhala masiku atatu wosadya kapena kumwa kanthu kalikonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nampatsanso cigamphu ca ncinci ya nkhuyu ndi ncinci ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wace unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya cakudya, osamwa madzi.