1 Samuel 30:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adafunsa munthuyo kuti, “Kodi iwe ndiwe munthu wa yani? Ndipo ukuchokera kuti?” Munthuyo adati, “Ndine Mwejipito, kapolo wa Mwamaleke. Mbuyanga adandisiya masiku atatu apitaŵa poti ndinkadwala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Davide ananena naye, Ndiwe wa yani? Ufumira kuti? Nati iye, Ndili mnyamata wa ku Ejipito, kapolo wa Mwamaleke; mbuye wanga anandisiya, chifukwa ndinayambodwala apita masiku atatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anafunsa kuti, “Kodi ndiwe yani, ndipo ukuchokera kuti?” Iye anayankha kuti, “Ine ndine Mwigupto, kapolo wa Mwamaleki. Mbuye wanga anandisiya nditayamba kudwala masiku atatu apitawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Davide ananena naye, Ndiwe wa yani? ufumira kuti? Nati iye, Ndiri mnyamata wa ku Aigupto, kapolo wa M-amaleki; mbuye wanga anandisiya, cifukwa ndinayambodwala apita masiku atatu.