1 Samuel 30:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tinkathira nkhondo dera la kumwera kwa Yuda, ku maiko a Akereti, ndi dera la Akalebe. Mwakuti tidatentha mzinda wa Zikilagi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tinathira nkhondo kumwera kwa Akereti ndi ku dziko lija la Ayuda, ndi kumwera kwa Kalebe; ndipo tinatentha mudzi wa Zikilagi ndi moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ife tinathira nkhondo dera la kummwera kwa mayiko a Akereti, dera la Yuda, ndi dera la kummwera kwa mayiko a Kalebe. Mzinda wa Zikilagi tinawutentha ndi moto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tinathira nkhondo kumwera kwa Akereti ndi ku dziko lija la Ayuda, ndi kumwera kwa Kalebi; ndipo tinatentha mudzi wa Zikilaga ndi moto.