1 Samuel 30:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adamufunsa kuti, “Kodi ungandiperekeze ku gulu lankhondo limenelo?” Munthuyo adati, “Muyambe mwalumbira kwa Mulungu kuti simundipha kapena kundipereka kwa mbuyanga. Mukatero ndikuperekezani ku gulu lankhondo limenelo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananena naye, Kodi udzanditsogolera kufikira ku khamulo? Nati iye, Mundilumbirire kwa Mulungu, kuti simudzandipha, kapena kundipereka m'dzanja la mbuye wanga, ndipo ndidzatsika nanu kuli khamu limene.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anamupempha kuti, “Kodi unganditsogolere kumene kuli gulu lankhondoli?” Iye anayankha kuti, “Mukandilonjeza molumbira kuti simudzandipha kapena kundipereka kwa mbuye wanga, ine ndikulondolerani kumene kuli gululo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika