1 Samuel 30:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho uja adaperekeza Davide kumeneko. Nthaŵi imeneyo Aamalekewo anali atamwazikana ponseponse. Analikudya, kumwa ndi kuvina, chifukwa cha zofunkha zimene adaatenga ku dziko la Afilisti ndi ku dziko la Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anatsika naye, onani, iwo anabalalika apo ponse, analinkudya, ndi kumwa, ndi kudyerera, chifukwa cha chofunkha zambiri anazitenga ku dziko la Afilisti, ndi ku dziko la Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwigupto uja anaperekeza Davide. Tsono Aamaleki anali atamwazikana ponseponse. Iwo ankadya, kumwa ndi kuvina chifukwa cha zofunkha zambiri zimene anatenga ku dziko la Afilisti ndi ku dziko la Ayuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anatsika naye, onani, iwo anabalalika apo ponse, analinkudya, ndi kumwa, ndi kudyerera, cifukwa ca cofunkha zambiri anazitenga ku dziko la Afilisti, ndi ku dziko la Yuda.