1 Samuel 30:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide ndi anthu ake adaŵathira nkhondo namenyana nawo kuyambira mbandakucha mpaka madzulo. Sadapulumukepo Mwamaleke ndi mmodzi yemwe, kupatula anthu 400 amene adakwera pa ngamira, nathaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anawakantha kuyambira madzulo kufikira usiku wa mawa wake; ndipo panalibe munthu mmodzi wa iwowa anapulumuka, koma anyamata mazana anai oberekeka pa ngamira, nathawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Davide anawakantha kuyambira madzulo atsikulo mpaka madzulo a tsiku linalo. Palibe anapulumuka kupatula anyamata 400 amene anakwera pa ngamira nʼkuthawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anawakantha kuyambira madzulo kufikira usiku wa mawa wace; ndipo panalibe munthu mmodzi wa iwowa anapulumuka, koma anyamata mazana anai oberekeka pa ngamila, nathawa.