1 Samuel 30:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panalibe kanthu kalikonse kamene kadasoŵapo. Adalanditsa ana aamuna ndi ana aakazi, ndiponso chilichonse chimene chidaatengedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sikanasoweka kanthu, kakang'ono kapena kakakulu, ana amuna kapena ana akazi, kapena chuma kapena china chilichonse cha zija anazitenga iwowa; Davide anabwera nazo zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe chimene chinasowa anthu onse, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, mnyamata mpaka mtsikana anapulumutsidwa. Davide anapulumutsa chilichonse chimene anafunkha Aamaleki aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sikanasoweka kanthu, kakang'ono kapena kakakuru, ana amuna kapena ana akazi, kapena cuma kapena dna ciri conse ca zija anazitenga iwowa; Davide anabwera nazo zonse.