1 Samuel 30:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatenga akazi kuti akhale akapolo, pamodzi ndi onse amene anali m'menemo, aang'ono ndi aakulu omwe. Sadaphepo ndi mmodzi yemwe, koma adaŵatenga amoyo napita nawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nagwira akazi ndi onse anali m'mwemo, akulu ndi ang'ono; sanaphe mmodzi, koma anawatenga, namuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anatenga akazi ndi onse amene anali mʼmenemo akuluakulu ndi angʼono omwe kuti akakhale akapolo. Sanaphe aliyense koma anawatenga amoyo napita nawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nagwira akazi ndi onse anali m'mwemo, akuru ndi ang'ono; sanapha mmodzi, koma anawatenga, namuka.